Mawu a Chikhulupiriro
Ndikhulupirira Mulungu Atate wa mphamvu zonse (yonse),
wakulenga za kumwamba ndi za pansi.
Ndikhulupirira Yesu Khristu, Mwana wake wobadwa yekha,
Ambuye wathu (Ambuyathu), amene anapatsidwa ndi (mwa) Mzimu Woyera,
nabadwa ndi Mariya namwaliyo, nasautsidwa kwa Pontio Pirato, namwalira (nafa),
naikidwa m’manda, natsikira kwa akufa (helo).Tsiku lachitatu anaukanso
kwa akufa, nakwera Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu Atate
wa mphamvu zonse (yonse), kuchokera (kudzera) komweko adzadza
kudzaweruza anthu amoyo ndi akufa.
Ndikhulupirira Mzimu Woyera. Ndikhulupirira Mpingo
wopatulika wa Khristu (wa Mulungu woyera) wa kwa anthu onse, chiyanjano
cha oyera mtima, kukhululukidwa kwa machimo, kuukanso kwa thupi, ndi
moyo wosatha.
Copyright © 2002 - Reproduced by
permission of Dr. Steven Paas